Home Local News KUCHEZA_NDI_YOBU_BAZALE_KACHITENJI

KUCHEZA_NDI_YOBU_BAZALE_KACHITENJI

by Harris Msosa
649 views

Yobu Bazale Kachitenji anabadwa pa 1 January 1999 ndipo m’banja la kwawo anabadwa ana 5 ndipo iye ndi wa number 4.

Yobu anayamba kuyimba m’chaka cha 2017 ndipo pa chiyambi ankayimba kwaya pa umwana wake ndipo mukuimba kwaya amakonda kumvera nyimbo za malemu Grace Chinga komanso Ester Chembekeza ndipamene anayamba kupeka nyimbo zoyimba payekha.

Mwezi watha watulutsapo nyimbo imodzi yomwe ikutchedwa kuti “Amasamala” ndipo mwezi uno akutulutsa nyimbo ina yomwe mutuwake ikutchedwa kuti “Amakhumudwitsa” zomwe zili
nyimbo zowonjezela panyimbo zina kuti chimbale chake chidzakwane chomwe akuyembekezela kudzatulutsa mtsogolo muno.

Yobu amakhala ku Mponela boma la Dowa ndipo sagwila ntchito iliyonse koma amapanga chabe business.

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media