Home Artist BiographyDan Mwananune Likhomo – Biography

Dan Mwananune Likhomo – Biography

by Kuwala Gospel Music
21 views

Dan Mwananune Likhomo ndi mwana wa a muchose Likhomo omwe anachokela kwa Nasoko ku Phalombe,ndipo anachoka kumeneko nakazipezera malo ku Machinga m’mudzi wa Kwilasha pafupi ndi Malape.Dan M.Likhomo adabadwa m’chaka cha 1973.

Dan ndi mulomwe ndithu ndipo m’banja mwao  anabadwamo ana 12 amuna 7 akazi 5 ndipo Dan ndi wa nambala 6 pakubadwa koma pano anatsala ana 8 akazi 4 amuna 4 ndipo ana 4 ndi makolo onse anamwalira.

Dan ndi munthu owopa Mulungu ndithu kuyambila ali m’nyamata  komaso ofatsa ndipo alibe kudana ndi munthu.Dzina la Mwananune ndilozichepetsesa ndithu.

Dan anayamba kuyimba m’chaka cha 2003 ndipo wakhala nthawi yaitali osatulutsa chimbale kamba koyenda yenda koma nyimbo zinalibe zikuwila m’mutu mwake tsono pamene danga layamba kupezeka mpamene wayamba kutulutsa nyimbozi ndipo pano wajambulitsa kale nyimbo zosachepela 30 ndipo watenga nyimbo 15 kupanga chimbale chotchedwa Chiukitso volume 1 komaso vulume 2 ndiyojambulidwa kale.

You may also like