Contacts:0886990639/0991981177/0882903634
Facebook Page:Canaan C.O.C Choir
Canaan C.O.C Choir ndi gulu loimba nyimbo za uzimu lomwe limapezeka ku Blantyre dela la Chigumula mudzi mwa a Chiswe T/A machinjiri.
Gulu limeneli ndi la pa mpingo wa Canaan Church of Christ omwe uli dela lomweli motsogozedwa ndi abusa a A.Gomesi.
Gulu la Canaan linayamba 2012 ndipo pofika pano lili ndi chimbale chimodzi cha nyimbo zomvela komatso zoonela chomwe anatulutsa mu 2022 chotchedwa MUKHALE NANE chomwe chili ndi nyimbo zokwana khumi.
Gulu limeneli lili ndi ma members okwana 26 omwe ali ndi zaka za pakati pa 7 to 35 omwe ali atsikana komaso anyamata.
Gulu la Canaan kupatula kuimba limagwiranso ntchito za Chifundo monga kuthandiza okalamba,amasiye,andende komanso athu ena omwe agweredwa mavuto osiyana siyana.
Gulu limeneli limachita ma business osiyana siyana pofuna kupeza thandizo lothandizila gulu lawo monga kuchita ulimi wa ziweto,njinga za kabaza ndi zina zambiri.
Pofika tsiku la lero gulu la Canaan C.O.C lilibe olithandizila pa chuma limazithandiza lokha.