Home Local News LITAH_LUBANO_NINE_WATULUTSA_ NYIMBO_YATSOPANO_LERO

LITAH_LUBANO_NINE_WATULUTSA_ NYIMBO_YATSOPANO_LERO

by Kuwala Gospel Music
811 views

Oyimba wina wa nyimbo za uzimu m’dziko muno yemwe amakhala ku Johannesburg m’dziko la South Africa Litah Lubano Nine watulutsa nyimbo yatsopano yotchedwa ndavomera lero.

Nyimbo ya ndavomera yomwe ndiyabwino komanso yotsitsimutsa ikukamba za kuvomera mayitanidwe a Mulungu. Nyimboyi yajambulidwa mwapamwamba komanso mwaukatswiri kwambiri ku Slate Music Records ndi Alex Chilambula ndipo ikupezeka pa malawigospelmusic.com.

Pomufunsa Litah za mawu ake otsiriza iye adalimbikitsa anthu omwe akumutumikira Mulungu kuti asatope kamba koti pakadali pano anthu atangwanika ndi zinthu zam’dziko.

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media