Alex Gomez K. Gondwe anayamba kuyimba mu chaka cha 2018 ndipo kufikira pano watulutsako ma single ake okwana awiri pamene nyimbo zake zina zitatu akuyembekezera kuzitulutsa mwezi wa mawa.
“Ndinali ndi chidwi kuyambira ku school ku secondary ndimayimba mu SCOM komanso ku Tchalitchi” Anatero Alex.
“Masophenya anga ndikufuna nyimbo zanga zimveke international” anapitiliza kulankhula motero Alex. Alex anati patenga nthawi kuti afike pochikhazikitsa chimbale chake chomwe wati adzachikhazikitsa mu mwezi wa October chaka chino.
Alex ndi mwana oyamba kubadwa mu banja la ana 4 ndipo pakadali pano akukhalira ku Benoni m’dziko la South Africa.
