Home “NDIKUFUNA ZIKADZANDIYENDERA NDIDZAFIKILE OMWE DZIKO SILIKUWAFIKILA NDI THANDIZO KUPHATIKIZAPO ANA AMASIYE NDI OLUMALA” MLALIKI STEVEN KALONGA.

“NDIKUFUNA ZIKADZANDIYENDERA NDIDZAFIKILE OMWE DZIKO SILIKUWAFIKILA NDI THANDIZO KUPHATIKIZAPO ANA AMASIYE NDI OLUMALA” MLALIKI STEVEN KALONGA.

by Kuwala Gospel Music
90 views

Steven Kalonga ndi mlaliki pa mpingo wa New Life Christian Church amene amayimba nyimbo za uzimu kuchokera ku Mzimba koma kumudzi kochokera ndi ku Ntcheu.

Mlaliki Steven adatulutsapo chimbale chimodzi m’chaka cha 2021 komanso DVD m’chaka cha 2022 ku studio ya Alimoso ku Mbayani koma kamba kavuto la ndalama sanathe kuchikhazikitsa chimbalechi.

Muchimbale choyamba muli nyimbo ten ndipo panopa akujambula chimbale chachiwiri chomwe chajambulidwa ma studio atatu osiyana ndipo nyimbo zina wajambula ndi Evance Watsopano Meleka, DJ Lobodo komanso Khatthwa Aligiza.

“Masomphenya omwe ndiri nawo ndiwoti ngati zitandiyendera ndidzafikile omwe dziko silikuwafikila ndi thandizo kuphatikizapo ana amasiye ndi olumala”. “Ndikufuna nditadzathandiza oyimba omwe akuvutika ndi luso lawo kuti asadzavutike ngati ineyo”. Adatero Mlaliki Steven.

Mlaliki Steven ndi wanambala 8 kubadwa mu banja la ana ten, anayi anyamata ndipo six akazi ndipo omwe ali moyo ndi 7 ndipo makolo onse anamwalira. Mlaliki Steven amakhala kukalikumbi mu boma la Mzimba.

Leave a Comment

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media