Promise Dawe anayamba kuyimba mu chaka cha 2004 koma anayamba kuwonekera ku athu mu chaka cha 2021 ndipo anatulutsako chimbale chimodzi mu chaka cha 2023.
“Ndimafuna ndidzakhale othandiza ma upcoming artist omwe amakhala osowekela thandizo mu music yawo” anatero Promise poyankha funso lakuti masomphenya ake ndi otani.
Promise akuganiza zotulutsa chimbale chachiwili chaka cha mawa mu November, Promise ndi mwana oyamba kubadwa mu banja la ana asanu koma pakadali pano anatsala ana atatu ndipo kwawo kwa Promise ndiku Lilongwe koma pakadali pano akukhalira m’dziko la South Africa.
