Fainess Bonface anabadwa komanso kukulira ku Ntcheu m’mudzi mwa Atimvere.Anabadwa pa 14 May,1990 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 7 koma ena anabadwa awiri (ma twins) ndipo iye ndi wa number 3 pobadwa.
Fainess amkapemphera mpingo wa Seventh Day Adventist nthawi imeneyo koma chifukwa cha mamuna yemwe anapeza pano amapemphera ku C.C.A.P ndipo ndi mzimayi wamvano.
Mayitanidwe amayimbidwe adamufikira ali kale pabanja koma kufika powonekera wayamba kupezeka mu chaka chomwe chino cha 2025 pomwe watulutsa album yake yotchedwa Nyengo zako zisitha ndipo anadalitsika ndi ana anayi, amuna atatu ndi wamkazi m’modzi, ena anabadwanso awiri (ma twins) mayina awo ndi Henderson, Harriet, Harvey ndi Harry.Fainess anasiyana ndi bambo a ana ake mu chaka cha 2023 ndipo pano aliyekha.