Lucas Bonongwe anabadwa komanso kukulira ku Mwanza m’mudzi mwa Nchotseni T/A Kanduku pa 21 January,1990 ndipo m’banja mwawo anabadwamo ana awiri koma pano anatsala Lucas yekha kamba kokuti winayo anamwalira ndipo iye ndi oyamba kubadwa.
Lucas atabadwa adapatsidwa dzina loti Luka ndipo anthu akhala akumudziwa ndi dzina loti Luka koma chifukwa cha zifukwa zina atayamba kukula anasintha dzina lija loti Luka mkumadzitcha kuti Lucas, mayi ake komanso abambo ake a Lucas anamwalira kalekale ali standard 1 ndipo iye wakula ndi anthu oti si azibale ake.
Lucas wakula akupanga ma sewelo pa school imene amaphunzila ndipo wakhala akuyenda ndi oyimba osiyanasiyana monga Davie Nsaku komanso James Chimoto.
M’chaka cha 2007 Lucas anachoka ku mwanza kubwera ku Blantyre kumene amakhala ndi anzawo a makolo ake ndipo sanatenge nthawi yayitali anayamba kulemba nyimbo ndipo mkupita kwa nthawi anadzatengedwa ndi oyimba wina otchuka amene amamuthandiza kuti luso lamayimbidwe lake lipite patsogolo.
M’chaka cha 2011 Lucas anaganiza zoyamba kulemba nyimbo za uzimu chifukwa nthawi imene amakhala kapena kuti kuthandizidwa ndi oyimbayu anali akuyimba nyimbo zachikunja ndipo anajambula chimbale chake choyamba chotchedwa kuti Palibe ofanana nanu, chimbale chimenechi anachikhazikitsa ku Mangochi mu chaka cha 2017 ndipo kumeneko kunali oyimba osiyanasiyana kuphatikizapo Evance Meleka. Pakadali pano Lucas ali ndi ma Album atatu m’mene muli nyimbo za uzimu.Lucas amakhala ku Machinjiri Area 2 ndipo amagwira ntchito ku Access komanso amapanga business.
