Steven Kalonga anabadwa m’chaka cha 1982 pa 21 September pachipatala cha Kamuzu Central,ndipo anabadwa mubanja la bambo Yohane Witness Kalonga ndi mayi Alena Mugabi m’mudzi wa Kapulula ku Ntcheu.
Bambo ake ankagwira ntchito ya ukhuki kufikila imfa yawo m’chaka cha 2021.Steven Kalonga anabadwa mubanja la ana khumi ndipo iyeyu ndi wa number 8, anayi amuna pomwe asanu ndi m’modzi anali akazi panopa atatu anamwalira pamodzi ndi makolo awo.
Sukulu yawo ya primary anamphunzira pa Loudan Primary kenaka anakaphunzira pa Livingstonia nights muchaka cha 2001 kenaka anasuntha ndikukalembera fomu 4 pa Mbawa Community Day Secondary School m’chaka cha 2004.Steven Kalonga ndiwokwatira ndipo ali ndi ana 4.Luso loyimba linayamba ali wachichepere zedi pomwe banja lakwawo linkakonda kumayimba nthawi yamadzulo tsiku ndi tsiku.Mumoyo wake onse sanasiyepo kumayimba nyimbo zosiyanasiyana kuphatikiza kukonda oyimba akuluakulu omwe ankamusangalatsa kwambiri monga Sir Paul Banda and Allelluyah Band, Soldier Lucius Banda, Coss Chiwalo,Paul Subiri and Rodrick Valamanja, Billy Kaunda, Wendy Harawa,Mlaka Maliro, Charles Sineta San B ndi ena. Apa ndipomwe chidwi choyimba chinakula kwambiri ndipo 2005 anakwanitsa kupeza 3000 yomwe anakajambula nyimbo imodzi kwa Ralph Ching’mba yotchedwa Nkhuzomera koma sinadziwike.M’chaka cha 2007 anakajambulanso single kwa malemu Joseph Tembo yotchedwa Changa Ndinyamaso koma sinadziwikenso apa mtima oyimba unachoka chifukwa chosowa thandizo.
Mu chaka cha 2007 analembedwa ntchito ngati mulonda pa company ya zitsime ya Marion Medical Mission yomwe inkatchedwa Shallow Well koma m’chaka cha 2008 mu August anasiya ntchitoyo ndikupita ku South Africa komwe anakagwira ntchito ngati Garden boy,ndi laundry man ndipo mu chaka cha 2009 anabwerako ku South Africa ndikuyamba kulima kwinako akumapanga maganyu osiyanasiyana kuphatikizapo kuwotcha chips ndikugulitsa feteleza oyeza.
M’chaka cha 2013 anapeza mwayi pa Chipatala cha mission cha Embangweni ngati Watchman kenako anamukweza pantchitopo ngati Patient Attendant m’chaka cha 2015, kenako anamupanga transfer kupita ku Health Center ya Kalikumbi m’chaka cha 2020 komwe akugwira ntchito yogawa mankhwala ku Pharmacy mpaka pano.
M’chaka cha 2021 ndipomwe anajambula album yoyamba ku Alimoso Studios DVD komanso audio ndi Khatthwa Aligiza ndi Moffat Aligiza, ndipo chimbale cha chiwiri chinajambulidwa ndi Khatthwa Aligiza,Evance Meleka ndi DJ Lobodo.
Steven Kalonga amatchulidwanso kuti Mlaliki Steven Kalonga, iyeyu anaphunzira pa School of Ministry ndi Kudzodzedwa ngati Pastor ndi Pastor Esau Banda a founder a PICC ku Lilongwe ndipo panopa amatumikila mu mpingo omwe unawatumiza ku school wa New Life Christian Center ku branch ya kukalikumbi ndipo panopa amakhala kukalikumbi ku Mzimba.