Home Artist Biography SYLVIA SHABA – BIOGRAPHY

SYLVIA SHABA – BIOGRAPHY

by Kuwala Gospel Music
90 views

Sylvia Shaba oyimba wa ku Malawi amachokera M’boma la Mzimba ndipo anabadwa  pa 13 September, 1984 ndipo wakulira ku Mzimba komko dera la  Manyamula m’mudzi mwa Zikhole Sakala.

Mu banja mwawo anabadwa ana 6 otsala atatu omwe anamwalira atatunso. Kwa iyeyu kuyimba ndi mayitanidwe kuchokera ali wachichepere, nthawi yomwe anali wachichepere ankakonda zoyimba monga ma choirs komanso ma fellowship.

Sylvia ali ku school atakwanitsa zaka 11 analota maloto oti ali pakati pa chimzinda chachikuru  akuyambitsa nyimbo yoti ndilandireni ine mbuye komanso nyimbo ina yotchedwa Hallelujah mwakuti  anachikhazikitsa pansi pa mtima wake kuti iye adzatumikira Mulungu moyo wake onse.

Sylvia wayimbapo ndi ma choirs ambiri moti mwa ena anaturutsa nawo chimbale monga  Manyamula Manse Choir ndi ma Band ena mu dela la Rumphi Mpherembe ndipo pachimenechi Sylvia analimbikitsidwa kuziyimira payekha mkuturutsa ma audio ake. 

Sylvia ndi mayi oti ali ndi ana  awiri ndipo oyamba   ali ndi zaka 19 pomwe wachiwiri  ali ndi zaka 15 ndipo poonjezera apo amasamaliranso ana atatu omwe ndi a malemu sister wake kusonyeza ali ndi ana 5 ndipo Sylvia ndi single Mom ndipo akukhala ku Durban North City m’dziko la South Africa ndipo ndikumene waturutsila ma audios ake.

You may also like

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media