Favour Chimpini Mkwamba anabadwa pa 5 /12/1995 ku Blantyre komaso kukulira Ku Blantyre komweko ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 8 koma omwe adatsala amoyo ndi 7 m’modzi adamwalira ndipo iye ndiwa number 6 pobadwa.
Atangobadwa adapatsidwa dzina loti Pilirani ndipo atabatizidwa adamupatsa dzina loti Favour.Mayitanidwe amayimbidwe adamufikira ali wachichepele kwambiri koma kufika pa air adayamba kupezeka mu 2022 pomwe anatulutsa single yake yotchedwa Sindidzaopa ndipo ali pa banja komanso anadalitsika ndi ana atatu wamamuna m’modzi a akazi awiri maina awo Chisomo, Lucy komanso Cosmas Mkwamba.Dzina loti Favour Chimpini ndilomwe anthu ambiri amamudziwa nalo.