Mike Wiseman Tembo anabadwa pa 1 January 1989 Ku Chilimba Nkairo ndipo akulira kuchilimba komweko ndi Ku Nsanje pa Phokera T/A Mbenje chifukwa mayi ake anachita kulowoledwa koma pano amakhalira kwa Bvumbwe T/A Bvumbwe ndipo ntchito amagwilira Ku South Africa in Soweto.
Maitanidwe amaimbidwe anayamba kale kupeka nyimbo 2005 Koma kujambura anayamba 2008 ndipo anajambulapo nyimbo zitatu monga, Mapiko,Mwaphera Njiru,Nkwabwino ndipo anajambula Ku studio ya bambo ake a Grace Chinga m’menemo mkuti akuyamba kumene imatchedwa Thanthwe Studio.M’chaka cha 2012 Mike Wiseman Tembo anapita Ku South Africa.
Mike Wiseman Tembo ndi m’busa ndipo amkakonda kutumikira moti anayamba kudziwa kularika ali ndi zaka 14 Koma maphunziro a ubusa anapanga 2016 pa college ina Kwa Bvumbwe yotchedwa New Covenant Bible College ndipo anapanga maphunziro a zaka zitatu nkupasidwako diploma.
Atafika zaka 15 anazisintha dzina kukhara Mike mpaka pano dzina lake ndi Mike Wiseman Tembo watsopano ndilomwe akugwiritsa ntchito.M’banja lawo anabadwa ana 9 koma pano anatsala 5.
Nyimbo zake amajambulitsa ku Malawi ngakhalenso ku South Africa komwe akukhalira pakadali pano.